Msilikali wa Malawi Defence Force komanso mkulu wina wowona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno amangidwa ku Karonga kamba kothandizira anthu asanu a mdziko la Ethiopia kulowa mdziko muno opanda zikalata zoyendera.
Mneneri wa polisi chagawo cha kumpoto , Maurice Chapola wasimikiza zakumangidwa kwa nathuwao ndipo watiso munthu wamba yemwe adasunga anthu olowa mosaloledwa m’nyumba mwake atathandizidwa ndi achitetezo awiriwa, wamangidwanso.
Chapola wati msilikaliyo ndi Lance Corporal, Brown Juma Phiri yemwe amagwira ntchito ku Chilumba barracks ku Karonga, ndi Sergeant Dayton Msukwa yemwe amagwira ntchito ku nthambi yowona anthu wolowa ndi kutuluka m'dziko m'no.
Polankhula ku Chinsowolo ground ku Karonga sabata yatha, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera anachenjeza kuti akuluakulu aboma athana ndi aliyense amene angathandize anthu kulowa m’dzikolo popanda chilolezo.
Masabata awiri apitawa, anthu opitilira 140 analowa m'dziko m'no